6 Tsopano tabwerani chonde, mudzatemberere anthuwa+ chifukwa ndi amphamvu kuposa ineyo. Mwina ndingawagonjetse nʼkuwathamangitsa mʼdziko lino, chifukwa ndikudziwa kuti munthu amene inu mwamudalitsa, amakhaladi wodalitsika, ndipo munthu amene mwamutemberera, amakhaladi wotembereredwa.”