6 Koma mwadzidzidzi anthuwo anangoona mwamuna wina wa Chiisiraeli akubwera ndi mkazi wa Chimidiyani.+ Anabwera naye kufupi ndi abale ake, pamaso pa Mose ndi gulu lonse la Aisiraeli. Pa nthawiyi nʼkuti Aisiraeliwo akulira pakhomo la chihema chokumanako.