18 chifukwa akubweretserani tsoka mochenjera pokukopani kuti muchimwe ku Peori.+ Muwaphe ndithu, chifukwanso cha zochita za mchemwali wawo Kozibi, mwana wa mtsogoleri wa ku Midiyani, amene anaphedwa+ pa tsiku limene mliri unakugwerani chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”+