12 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Nyamuka, tsika mofulumira mʼphiri muno, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa ku Iguputo achita zinthu zoipa.+ Apatuka mofulumira panjira imene ndinawalamula kuti aziyendamo. Adzipangira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo.’+