6 Nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu,+ nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo, nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzapita nazo kumalo amenewo.+