15 Ngati mukufuna kudya nyama, mungathe kupha chiweto chanu nʼkudya nyama yake nthawi iliyonse,+ mogwirizana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani mʼmizinda yanu yonse. Munthu wodetsedwa komanso munthu wosadetsedwa angathe kudya nyamayo, ngati mmene mungadyere insa ndi mbawala.