26 Ndalamazo muzidzagulira chilichonse chimene mtima wanu wafuna, kaya ndi ngʼombe, nkhosa, mbuzi, vinyo, chakumwa choledzeretsa ndi chilichonse chimene mtima wanu wafuna. Ndipo muzidzadya zinthuzi pamaso pa Yehova Mulungu wanu nʼkusangalala, inuyo ndi banja lanu.+