2 Muzichita izi pomasula anthu angongolewo: Munthu aliyense azimasula mnzake amene ali ndi ngongole yake. Asamakakamize mnzake kapena mʼbale wake kuti abweze ngongoleyo, chifukwa chilengezo choti anthu angongole amasuke chaperekedwa potsatira lamulo la Yehova.+