6 Akapanda kutero, chifukwa chakuti wobwezera magazi+ ndi wokwiya kwambiri, angathamangitse wopha munthuyo nʼkumupeza kenako nʼkumumpha chifukwa chakuti mtunda wopita kumzindawo unali wautali. Koma wopha mnzake mwangoziyo samayenera kufa chifukwa sankadana ndi mnzakeyo.+