19 Mukazungulira mzinda nʼcholinga choti muulande ndipo mwakhala mukumenyana nawo kwa masiku ambiri, musawononge mitengo yake poidula ndi nkhwangwa. Mukhoza kudya zipatso za mitengoyo, koma simukuyenera kuidula.+ Kodi mtengo wamʼmunda ndi munthu kuti muwuukire?