21 azibweretsa mtsikanayo pakhomo la nyumba ya bambo ake ndipo amuna amumzindawo azimuponya miyala kuti afe, chifukwa wachita chinthu chochititsa manyazi mu Isiraeli,+ pochita chiwerewere mʼnyumba ya bambo ake.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+