14 Sindinadyeko zina mwa zimenezi pa nthawi imene ndinali pa chisoni, kapena kutengapo zina mwa zimenezi ndili wodetsedwa, kapena kupereka zina mwa zinthu zimenezi chifukwa cha munthu wakufa. Ndamvera mawu a Yehova Mulungu wanga ndipo ndachita zonse zimene munandilamula.