16 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri za padziko lapansi, ndi chuma chake chonse,+
Komanso movomerezedwa ndi Iye amene anaonekera mʼchitsamba chaminga.+
Madalitso amenewa akhale pamutu pa Yosefe,
Paliwombo pa munthu amene anasankhidwa pakati pa abale ake.+