14 Akazi anu ndi ana anu atsale limodzi ndi ziweto zanu kutsidya lino la Yorodano,+ pamalo amene Mose wakupatsani. Koma asilikali amphamvu nonsenu,+ muwoloke ndipo muzikayenda patsogolo pa abale anu,+ mutakonzeka kumenya nkhondo. Muyenera kuwathandiza.