23 Choncho, anyamata amene anakafufuza zokhudza dziko aja, anapita kukatulutsa Rahabi limodzi ndi bambo ake, mayi ake, azichimwene ake ndi onse amene anali naye. Anatulutsa achibale ake onse,+ ndipo anayenda nawo bwinobwino kupita nawo kumalo ena kunja kwa msasa wa Isiraeli.