13 Dzuka ndipo uyeretse anthuwa.+ Uwauze kuti, ‘Mudziyeretse pokonzekera mawa, chifukwa Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Anthu inu pakati panu pali zinthu zoyenera kuwonongedwa. Simudzathanso kulimbana ndi adani anu, pokhapokha mutachotsa zinthu zoyenera kuwonongedwazo.