14 Mawa mʼmawa, mubwere mafuko onse. Fuko limene Yehova adzasankhe+ lidzabwera patsogolo. Kenako mbumba ndi mbumba, ndipo mbumba imene Yehova adzasankhe idzabwera patsogolo. Kenako banja ndi banja, ndipo banja limene Yehova adzasankhe lidzabwera patsogolo, kenako mwamuna aliyense payekhapayekha.