-
Yoswa 8:33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Aisiraeli onse, atsogoleri awo, akapitawo awo, ndi oweruza awo anasonkhanitsidwa pamodzi. Panalinso alendo ndi nzika.+ Ena anaima mbali iyi ya Likasa, ena anaima mbali inayo, pamaso pa Alevi omwe anali ansembe amene ananyamula likasa la pangano la Yehova. Hafu ya anthuwo inaima mʼphiri la Gerizimu, ndipo hafu ina inaima mʼphiri la Ebala,+ (ngati mmene Mose mtumiki wa Yehova analamulira),+ kuti Aisiraeliwo adalitsidwe.
-