24 Anthuwo anayankha Yoswa kuti: “Akapolo anufe tinauzidwa mosapita mʼmbali kuti Yehova Mulungu wanu analamula mtumiki wake Mose kuti akupatseni dziko lonseli ndiponso muphe anthu onse okhalamo.+ Choncho tinachita mantha kuti mutipha.+ Nʼchifukwa chake tinachita zimenezi.+