30 Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Isiraeli.+ Choncho Aisiraeli anapha anthu onse amumzindawo ndi lupanga, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Libina anaichita zofanana ndi zomwe anaichita mfumu ya ku Yeriko.+