39 Analanda mzindawo ndi midzi yake yonse nʼkugwiranso mfumu yake. Ndiyeno anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mmenemo+ ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka.+ Anachitira mzinda wa Debiri ndi mfumu yake zimene anachitira mzinda wa Heburoni komanso mzinda wa Libina ndi mfumu yake.