40 Choncho Yoswa anagonjetsa anthu amʼdera lonse lamapiri, anthu a ku Negebu, a ku Sefela,+ ndi amʼmadera otsetsereka pamodzi ndi mafumu awo onse. Anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka ndipo anapha chamoyo chilichonse+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wa Isiraeli analamula.+