2 Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni ndipo ankalamulira kuyambira kumzinda wa Aroweli,+ womwe unali mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni+ komanso kuyambira pakatikati pa chigwachi, ndi hafu ya Giliyadi mpaka kukafika kuchigwa cha Yaboki, kumalire ndi Aamoni.