27 Gawo lawolo linaphatikizaponso mizinda ya mʼchigwa ya Beti-harana, Beti-nimira,+ Sukoti,+ Zafoni ndi dera lotsala la dziko la Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.+ Mtsinje wa Yorodano ndi umene unali malire awo kuchokera kumunsi kwa nyanja ya Kinereti,+ kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano.