2 Ana a Manase otsalawo anapatsidwa gawo lawo motsatira mabanja awo. Gawolo linaperekedwa kwa ana a Abi-ezeri,+ ana a Heleki, ana a Asiriyeli, ana a Sekemu, ana a Heferi ndi ana a Semida. Amenewa anali ana aamuna a Manase mwana wa Yosefe, motsatira mabanja awo.+