47 Koma fuko la Dani gawo lawo linkawachepera,+ choncho anapita kukachita nkhondo ku Lesemu.+ Analanda mzindawo nʼkupha anthu ake ndi lupanga. Kenako anautenga nʼkuyamba kukhalamo ndipo anausintha dzina loti Lesemu nʼkuupatsa dzina loti Dani, potengera dzina la kholo lawo Dani.+