32 Mafupa a Yosefe,+ amene Aisiraeli anabweretsa kuchokera ku Iguputo anawaika mʼmanda ku Sekemu, pamalo amene Yakobo anagula kwa ana a Hamori,+ bambo wa Sekemu. Malowo anawagula ndi ndalama zasiliva zokwana 100,+ ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.+