16 Ndiyeno ana a munthu wamtundu wa Chikeni,+ yemwe anali mpongozi wa Mose,+ anatuluka mumzinda wa mitengo ya kanjedza+ pamodzi ndi anthu a ku Yuda nʼkukalowa mʼchipululu cha Yuda, kumʼmwera kwa Aradi.+ Ndipo iwo anayamba kukhala pamodzi ndi anthuwo.+