15 Kenako Aisiraeli anafuulira Yehova kuti awathandize.+ Choncho Yehova anawapatsa mpulumutsi,+ Ehudi+ mwana wa Gera. Ehudi anali munthu wamanzere+ ndipo anali wa fuko la Benjamini.+ Patapita nthawi, Aisiraeli anatumiza msonkho wawo kwa Egiloni mfumu ya Mowabu, ndipo Ehudi ndi amene anakapereka.