28 Amuna amumzindawo atadzuka mʼmawa, anaona kuti guwa lansembe la Baala lagwetsedwa, ndipo mzati wopatulika umene unali pambali pake wadulidwa. Anaonanso kuti paguwa limene lamangidwa, panali pataperekedwa nsembe ngʼombe yaingʼono yamphongo yachiwiri ija.