6 Aisiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ mafano a Asitoreti, milungu ya ku Aramu, milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya Aamoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Iwo anasiya Yehova ndipo sankamutumikira.