13 Ndiyeno mfumu ya Aamoni inauza anthu amene Yefita anawatumawo kuti: “Nʼchifukwa chakuti Aisiraeli analanda dziko langa atachoka ku Iguputo.+ Analanda dzikoli kuyambira ku Arinoni+ kukafika ku Yaboki mpaka kukafikanso ku Yorodano.+ Ndiye mubweze dzikoli mwamtendere.”