11 Zitatero, amuna 3,000 a ku Yuda anapita kuphanga la thanthwe la Etami nʼkuuza Samisoni kuti: “Kodi iwe, sukudziwa kuti Afilisiti ndi amene akutilamulira?+ Ndiye nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi?” Iye anawayankha kuti: “Ndawachita zimene iwo anandichitira.”