5 Zitatero olamulira a Afilisiti anapita kwa mkaziyo nʼkumuuza kuti: “Umunyengerere+ kuti udziwe chimene chimamuchititsa kuti akhale ndi mphamvu zambiri komanso zimene tingachite kuti timufoole, timʼmange ndiponso timugonjetse. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva zokwana 1,100.”