12 Ndiyeno Delila anatenga zingwe zatsopano nʼkumumanga nazo manja ndipo anamuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” (Pa nthawiyi nʼkuti anthu atamʼbisalira mʼchipinda china.) Samisoni atamva zimenezi anadula zingwe zimene anamʼmanga nazozo ngati akudula ulusi.+