-
Oweruza 16:30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Ndiyeno Samisoni anafuula kuti: “Ndife nawo limodzi Afilisitiwa!” Kenako anakankha zipilalazo ndi mphamvu zake zonse ndipo nyumbayo inagwera olamulira a Afilisiti ndi anthu onse amene anali mmenemo.+ Choncho anthu amene Samisoni anawapha pa nthawi ya imfa yake anali ambiri kuposa amene anawapha pa nthawi imene anali ndi moyo.+
-