-
Oweruza 18:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Choncho amuna 5 aja anapitiriza ulendo wawo ndipo anafika mumzinda wa Laisi.+ Anaona kuti anthu amumzindawo ankakhala mosadalira aliyense, ngati mmene ankakhalira Asidoni. Iwo ankakhala mosatekeseka+ ndipo panalibe amene anawagonjetsa nʼkumawalamulira mwankhanza kapena kuwasokoneza. Ankakhala kutali kwambiri ndi Asidoni ndipo sankayenderana ndi anthu ena.
-