9 Kenako mwamunayo anaimirira kuti azipita pamodzi ndi mkazi wake ndiponso mtumiki wake. Koma bambo a mtsikanayo, anamuuza kuti: “Komatu dzuwa lapendeka. Bwanji mugonenso? Kunjakutu kuda posachedwa. Gonani ndipo musangalale. Mawa mukhoza kudzuka mʼmawa nʼkumapita kunyumba kwanu.”