28 Pa mafuko onse a Isiraeli ndinasankha kholo lako+ kukhala wansembe wanga, kuti azipita paguwa langa lansembe+ kukapereka nsembe zanyama, azipereka nsembe zofukiza ndiponso kuti azivala efodi pamaso panga. Komanso ndinapatsa nyumba ya kholo lako nsembe zonse zotentha ndi moto za Aisiraeli.+