21 Iye anapatsa mwanayo dzina lakuti Ikabodi+ nʼkunena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina.”+ Ananena zimenezi chifukwa cha Likasa la Mulungu woona limene linali litalandidwa ndiponso chifukwa cha zimene zinachitikira apongozi ake ndi mwamuna wake.+