9 Ndiyeno muzikaliyangʼana: Likasalo likakalowera njira yopita kwawo ku Beti-semesi,+ ndiye kuti iye ndi amenedi watichitira zinthu zoipa kwambirizi. Koma ngati silikalowera kumeneko, tidzadziwa kuti si dzanja lake limene latichitira zoipazi, koma zangochitika.”