17 Zifaniziro zagolide za matenda a mudzi zimene Afilisiti anatumiza kwa Yehova monga nsembe yakupalamula ndi izi:+ Mzinda wa Asidodi+ unapereka chifaniziro chimodzi, wa Gaza chimodzi, wa Asikeloni chimodzi, wa Gati+ chimodzi ndiponso wa Ekironi+ chimodzi.