10 Pamene Samueli ankapereka nsembe yopsereza, Afilisiti anali akuyandikira kuti amenyane ndi Isiraeli. Zitatero, Yehova anachititsa mabingu amphamvu kwambiri+ pa tsiku limenelo kuti asokoneze+ Afilisiti. Choncho Afilisitiwo anagonjetsedwa ndi Aisiraeli.+