8 Kenako iye anaima nʼkuyamba kufuulira asilikali a Isiraeli+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwabwera nʼkuyalana kuti mumenye nkhondo? Ine ndabwera kudzamenyera nkhondo Afilisiti ndipo inu ndinu antchito a Sauli. Ndiye sankhani munthu woti amenyane nane ndipo abwere kuno.