23 Pamene ankalankhula ndi asilikaliwo, ngwazi ija inatulukira kuchokera pakati pa asilikali a Afilisiti. Dzina la ngwaziyo linali Goliyati,+ Mfilisiti wa ku Gati. Iye anayamba kulankhula mawu omwe aja amene analankhula poyamba,+ ndipo Davide nayenso anamva.