26 Davide anayamba kufunsa asilikali amene anali naye pafupi kuti: “Kodi munthu amene angaphe Mfilisitiyu nʼkuchititsa kuti Aisiraeli asiye kunyozedwa amupatsa chiyani? Kodi Mfilisiti wosadulidwa ameneyu ndi ndani kuti azinyoza asilikali a Mulungu wamoyo?”+