52 Zitatero, asilikali a Aisiraeli ndi Yuda anayamba kufuula ndipo anathamangitsa Afilisiti kuyambira kuchigwa+ mpaka kumageti a mzinda wa Ekironi.+ Mitembo ya Afilisiti amene anaphedwa inali mbwee mʼnjira monse kuchokera ku Saaraimu+ mpaka kukafika ku Gati mpaka ku Ekironi.