6 Davide ndi asilikali ena akamabwera kuchokera kokapha Afilisiti, azimayi ankatuluka mʼmizinda yonse ya Isiraeli akuimba nyimbo+ komanso kuvina. Iwo ankapita kukachingamira Mfumu Sauli mosangalala, akuimba maseche+ komanso choimbira cha zingwe zitatu.