10 Tsiku lotsatira, Sauli anagwidwa ndi mzimu woipa wochokera kwa Mulungu+ moti anayamba kuchita zinthu zachilendo mʼnyumba mwake. Pa nthawiyi nʼkuti Davide akuimba nyimbo ndi zeze+ ngati mmene ankachitira ndipo Sauli anali ndi mkondo mʼmanja mwake.+