3 Koma Davide analumbira kuti: “Bambo ako akudziwa kuti umandikonda.+ Choncho akhoza kunena kuti, ‘Yonatani musamuuze zimenezi chifukwa akwiya nazo.’ Moti ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, komanso pamaso pako, imfa ili pafupi kwambiri ndi ine!”+